Religion

Kusagwirizana kwabuka ku QMAM pamene amwenye akudzudzulidwa kuti akubweretsa chisokonezo

Kusagwirizana kwabuka pakati pa otsatira chipembedzo chachisilamu cha Qadria pamene opembedza achikuda akudzudzula opembedza anzawo achimwenye kuti akuwapondereza komanso akuwazunza.

Mwazina, opembedza achikudawa akuti amwenye akulowerera mzochitika za bungwe la Qadria Muslim Association of Malawi (QMAM) ndi cholinga chobweretsa kugawanikana pakati pa otsatira chipembedzochi.

Malingana ndi zomwe Sheikh Mhuyudeen watiuza kudzera mu mau omwe wajambula yekha, asilamu a chi Qadria ndi okhumudwanso kwambiri ndi chigamulo chomwe chinapelekedwa ku High Court ya Lilongwe pa 29 Feburary 2023 ya pakati pa The Registered Trustees ya QMAM ndi Sheikh Jaffar Kawinga komanso Brother Osman Kareem.

Ndipo kudzera mkalata yomwe ma Qadria okhudzidwa atiwonetsa, iwo akuti ichi ndi chifukwa chake agwirizana zokamang’ala ku bwalo lomaliza la milandu la Supreme.

“Aslamu a Qadria m’dziko muno akuti pachigamulochi panachitika zachinyengo zambiri, Mwachitsanzo: 1. Pa 30 August 2023 High Court ndipomwe lima maliza kumva mboni zambali zonse Ndipo Court kudzela mwa Judge Hon. Kenyatta Nyirenda Lidanenakuti Chigamulo Chankhaniyi chipelekedwa Mkati mwa 30 days. Chodabwitsa choyamba, panadutsa masiku osachepera 180 mmalo mwa 30.

“Chodabwitsa chachiwiri, kwa odandaula zoti chigamulo chiperekedwa pa 29 February 2024 sitinadziwe kufikira pa 28 February 2024 nthawi ya 5pm ndipomwe timamva anthu ena zoti chigamulo ndi mawa,” ikutero kalatayo

Kalatayo ikuti chodabwitsa chachitatu ndi choti patsikulo, anthu atasonkhana kuti akazimvere okha, koma adaletsedwa kulowa kupatula okhawo omwe amaperekela umboni pankhaniyi.

Iwo akuti adalinso odabwa kuwona kuti odandaulawa sadapatsidwe mpata ulionse kuti afotokoze mbali yawo, komanso chigamulocho sichinawerengedwe chonse monga zimafunikira kuti aliyense achimvetsetse.

“Ndiye Loya yemwe akuti yimilila pa Appeil imeneyi ndi Hon. TAULO & ……..Tikunenapano chilichonse chokhuza kuimitsa Chigamulo ndi kuchita Appeil zinapelekedwa kale Tikungodikila Court livomeleze zimenezi pofuna kulemekeza ma ufulu athu ngati ifenso m’dzika zeni zeni za m’dziko lino. Pali mphekezela zambiri zomwe zikumveka mbalizonse za dzikolino zoti Pali amwenye ena omwe akufuna kulanda bungwe la QMAM  kudzela mu anthu ogwira ntchito kuma bungwe awo monga IMARAT- ASUM- AQSA, Ndi anthu ena owelengeka adyela, kuti bungweli liziyendetsedwa  ndimalamulo Amwenye,” akutero Asilamu a Qadria’wa.

“Mwachoncho Anthuwa Akuwachenjeza Amwenye adyelawa kuti ngati sakukhutitsidwa ndizomwe amapeza m’mabungwe omwe alinawowa angofuna Business ina Asayambitse chisokonezo chapakati pa Aslamu a Qadria okha okha m’dziko muno. Achenjezanso Atsogoleli a bungwe la MUSLIM ASSOCIATION OF MALAWI (MAM) Kuti Alangize ma membala awo Asukuti omwe akufunitsitsa kulanda bungwe la QMAM motsogodzedwa ndi Sheikh Jaffar Kawinga kunenakuti apeze zina   zochita kusiyana ndikuti ayambitse nkhondo yapachiweniweni m’dziko muno Chifukwa Aslamu a Qadria Sitilola kuti Wa sukuti, kapena Membala wamachiya kuti atilamulile mubungwe la QMAM ayi Ndipo tilolela chilichonse chichitike Kuti Ufulu wathu wachipembedzo Usapondelezedwe,” ikutero kalatayi kumapeto kwake.

Pakadali pano, Shehe Mhuyudeen wamema otsatira chipembedzochi kuti akapange zionetsero potsutsana ndi ulamuliro wa QMAM, potsindika kuti amwenye akusokoza chilungamo ku bungweli.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button
Nthanda Times

Adblock Detected

Please consider supporting us by disabling your ad blocker